News

Amenyedwa ndi azilamu awo akazi mpaka kuwavulaza ziwalo

Mayi Dorica anamenyedwa ndi azilamu awo ataonetsa kusakondwa kuti amuna awo apeza mkazi wina

May Dorica Amos amene am’mudzi wa Liyapa Mfumu Yaikulu Mkanda m’boma la Mulanje ali mu ululu pa chipatala cha Queen Elizabeth Central ku Blantyre atamenyedwa ndi azilamu awo akazi.

Iwo ati adamenyedwa ndi azilamu awowa aakazi  anayi posakondwa kuti iwo [a Dorica] sanakondwe kuti amuna awowa adapeza mkazi wina.

A Dorica omwe pakadali pano ali ndi zaka 19 zakubadwa adachimwitsidwa ndi mlongo wawo wa amayi anayiwa pomwe adali ndi zaka 17 zakubadwa.

Iwo ali pa chipatala cha chikuluchi popeza avulala nsana ndi ziwalo zina chifukwa cha kumenyedwaku.

Related Articles

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *

Back to top button