
Paris Saint-Germain (PSG) yapambana ndi Arsenal 2-1 mu masewero a semi-final yachiwiri ya Champions League, ndikupita ku final ndi chiwerengero cha zigoli 3-1. Fabian Ruiz anachinya chigoli choyamba cha PSG kuchokera pa set piece yabwino kwambiri, pomwe Achraf Hakimi anachinya chigoli chachiwiri atathandizidwa ndi Ousmane Dembele. Bukayo Saka ndiye anachinya chigoli chokhalo cha Arsenal pa masewerowa.



