News

Evance Meleka wakana zoti wamenyedwa

Mmodzi mwa oyimba nyimbo zauzimu, Evance Watsopano Meleka, watsutsa mpheketsera zomwe ena akufalitsa pa masamba a mchezo kuti uye wamenyedwa.

Meleka wati ndizodabwitsa kuti nthawi zambiri anthu akumakonda kumupekera nkhani zomwe ziri zabodza.

“Chilandirireni Yesu nkuyamba kutumikira Mulungu, nkhondo zoterezi zikuchuluka koma ndikudziwa kuti Satana samakondwa nane chifukwa choti ndinasiya kumutumikira,” iye watero.

Iye wati ulendo wina ena anafalitsanso kuti wamwalira ndipo ena anafalitsa kuti wamangidwa.

Meleka amadziwika ndi nyimbo monga Yanokola ndipo posachedwapa watulutsa nyimbo yomwe akuti Sapanganika.

Related Articles

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *

Back to top button