
Mtsogoleri wa dziko lino, Dr. Lazarus Chakwera, wati maboma amene adatsatira ulamuliro wa Dr. Hastings Kamuzu Banda adasokoneza masomphenya a dziko lino.
Iwo ananenanso kuti zinthu zimene Kamuzu Banda adasiya zolimbikitsa chitukuko, zinafooketsedwa ndi atsogoleri ena zomwe zidapangitsa kuti dziko libwerere m’mbuyo.
Mwachitsanzo, Dr. Chakwera adati ena atalowa m’boma adagulitsa ndi kutseka mafakitale, zomwe zinachititsa kuti anthu ambiri azisowa ntchito.
Komabe, Dr. Chakwera adati boma lawo likugwira ntchito molimbika kuti loto la Kamuzu Banda, mtsogoleri woyamba wa dziko lino, lisapitirire kukhala mbiri yokha, koma lichitike zenizeni.
Iwo ananena izi ku Mzuzu pa mwambo wokumbukira Dr. Hastings Kamuzu Banda.



